Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la Landnet Lapempha Boma Kukhazikitsa Lamulo Lokhudza Malo

$
0
0

Bungwe la Landnet Malawi lapempha boma kuti likhazikitse msanga lamulo lokhudza malo lomwe aphungu akhala akulephera kulikambirana kunyumba ya malamulo, pofuna kuchepetsa milandu yokhudza malo mdziko muno.

Mkulu oyendetsa ntchito za bungweli a Emmanuel Mlaka ndi omwe apereka pempholi bungweli litatengera atolankhani mmaboma a Chitipa, Karonga, Salima komanso Thyolo pofuna kuti akaziwonere okha mavuto omwe anthu akukumana nawo chifukwa chosowa lamuloli.

Iwo ati lamuloli, lingathandize kwambiri maka kwa anthu osauka omwe amalandidwa malo ndi anthu a chuma omwe amapondereza anthuwa mwanjira zosiyanasiyana kamba kosowa lamuloli.

A Mlaka ati malamulo okhudza malo akuyenera kukhala a mphamvu ponena kuti izi zithandiza mzika za dziko lino kuti zizikhala bwino ndikumanyadira boma lawo.

Pamenepa iwo  ati nkhani za malo ndi zachilengedwe zimafunika ziziyang’aniridwa bwino ponena kuti anthu omwe akusunthiidwa kupita ku madera ena akuyenera kupatsidwa zonse zoyenera kuphatikizapo chipukuta misozi kamba koti izi zingathandize kuthetsa mikangano ya pakati pa boma ndi anthu eni ake


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>