Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco,wapempha anthu kuti pamene mpingowu lachitatu umakumbukira odwala padziko lonse, akhale ndi nthawi yapadera yoyendera odwala, pofuna kuphunzirapo kanthu pa zamavuto omwe akukumana nawo.
Poganizira tsikuli, atsogoleri osiyanasiyana mu mpingo wakatolika mmadayosizi,mmaparishi ndi mmalo ena, akuyendera odwala mzipatala ndi mmalo ena padziko lonse, pofuna kuwawonetsa chikondi komanso kuwapatsa chiyembekezo powapemphelera ndi kugawana nawo zaulele za Mulungu.
Mtsogoleri wakale wampingowu padziko lonse malemu Papa Yohane Paulo wachiwiri Oyera, ndi yemwe anakhazikitsa tsikuli pa 13 May 1992, pofuna kufikira anthuwa mwapadera chaka chilichonse.
Muuthenga wa Papa Francisco okumbukira tsikuli chaka chino omwe mutu wake ndi oti“Ndinali ngati maso kwa anthu osawona” ndipo ngati phazi kwa anthu opunduka ochokera pa Yobu 29 ndine ya 15,Papa Francisco wapempha akhrisitu onse mumpingowu ndinso anthu ena akufuna kwabwino,kuti akhale ndi Nzeru Za Mumtima, zomwe angazigwiritse ntchito podziiwala iwo eni ndikuika patsogolo umoyo wa anthu ena maka amene akudwala matenda osiyanasiyana powayendera.
Iye wati masiku ano ndikosavuta kuiwala kufunika kwa nthawi imene munthu angatenge pochezera munthu amene akudwala ngakhale pakati pa anthu okhulupilira Mulungu,zomwe ati zikuchititsa kuti chikhulupiliro cha anthu mwa Mulungu chikhale chabodza.