Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mutharika Akhaziktsa Ndondomeko za Kayendetsedwe ka Ntchito za Boma

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika, wakhazikitsa ndondomeko zomwe zithandize nthambi zaboma kuyendetsa bwino ntchito zake.

Polankhula pa mwambo okhazikitsa ndondomekoyi ku Bingu International Conference Centre mu mzinda wa Lilongwe, Pulezidenti Mutharika wati nthambi zaboma, zimagwira ntchito yayikulu pachitukuko cha dziko, ndipo wati mpofunika kuti pakhale ndondomeko zabwino zomwe zithandize kuti nthambizi zizigwira ntchito zake mokonzeka kulimbana ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nawo, komanso amene angathe kuchitika mtsogolo.

Iye wati kwa nthawi yayitali, dziko lino lakhala likukambapo zofuna kukonzanso momwe nthambi zaboma zizigwirilira ntchito zake, koma wati palibe chomwe chimachitika, ndipo wati nthawi yakwana kuti nthambizi zigwire ntchito zake moyenera  kudzera mu ndondomeko yokonza kayendetsedwe ka nthambizi ya Public Service Reform Commission.

Zina mwa ntchito zomwe Pulezidenti Mutharika watchula pansi pa ndondomeko yokonzanso ntchito za nthambizi, zomwe zabereka kale zipatso zabwino ndi kukhazikitsidwa kwa ofesi zosindikiza ziphaso ku ofesi za Immigration ku Mzuzu ndi Lilongwe,komanso kuletsa alembi a mmaunduna boma kukhala nawo mmisonkhano ya Pulezidenti yomwe sikukhudzana ndi maunduna awo.

Wapampando wa nthambi ya Public Service Reform Commission ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulosi Chilima,omwe anenetsa kuti kagwiridwe ka ntchito munthambi zaboma kakuyenera kusinthidwa pofuna kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>