Likulu la mpingo wakatolika ku Vatican, lawuza bungwe la mgwirizano wa mayiko la United Nations,kuti mpingowu ndiwokhudzidwa kwambiri powona kuti kukwera kwa chuma mmayiko ena padziko lonse, sikukupindulira anthu mofanana mmayikowo.
Kazembe okhazikika wa mpingowu ku likululo pankhani za umoyo wa anthu Archbishopu Bernardito Auza,wanena izi atakumana ndi akuluakulu a munthambi yowona za umoyo wa anthu kubungwelo.
Archbishopu Auza, wati pamene mayiko akuyesetsa kuyika njira zosiyanasiyana zofuna kukwezera miyoyo ya anthu, chuma chopezeka mmayikowo kudzera mu njira zosiyanasiyana, sizikupindulira anthu mmayikowo mofanana.
Iye wati kuwonetsetsa kuti anthu ambiri akulembedwa ntchito kuti azidzipezera thandizo, sikokwanira,ndipo ati mpofunika kuti umunthu wawo udzilemekezedwa munjira zosiyanasiyana kuphatikizapo powapatsa zinthu zoyenera pamoyo wawo.
Iye wati mpofunika kuti mayiko, ayike chidwi chapadera pa anthu amene amaponderezedwa pofuna kuti adzipindula ndi phindu lomwe mayiko awo amapeza.