Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa Katolika Wafunira Akhristu Zabwino mu Nyengo ya Lenti

$
0
0

Mpingo wakatolika kuno ku Malawi wafunira akhristu komanso a malawi onse mafuno abwino,pamene lero ayamba ulendo wa masiku makumi anayi okumbukira masautso a Yesu Khristu.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi, ogwirizira udindo wa mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi mdziko muno Bambo Emmanuel Chimombo, apempha akhristuwa komanso onse akufuna kwabwino,kuti awonjezere mapemphero awo komanso kuchita ntchito za chifundo maka pano pamene anthu ena ali pamavuto aakulu chifukwa cha madzi osefukira.

Bambo Chimombo ati koposaposa, nyengo ya masautso a Yesu Khristu ikuyitana akhristu onse kuti akumbukire zoyipa zomwe zili mmitima mwawo ndikufunitsitsa kulapa, ndicholinga choti pakutha paulendo wa masiku makumi anayiwa,adzayambe moyo watsopano.

Iwo  apemphanso akhristu kuti apezerepo mwayi opemphelera mabanja pamene msonkhano wachiwiri  wa maepiskopi okambirana nkhani zokhudza banja ,ukuyembekezeka kuchitika mmwezi wa October chaka chino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>