Bozyolo Chigwenembe wa zaka 22 zakubadwa wadzipha podzimangilira pambuyo pokangana ndi mkazi wake kwa mfumu yaikulu Dzoole m’boma la Dowa.
Mneneli wa apolisi ku Mponela m'bomalo a Kondwani Kandiado ati Chigwenembe adadzipha podzimangilira kamba koti adasemphana mawu ndi mkaziyo, Bertha Nashe wa zaka 19 zakubadwa.
Mkaziyo amadwaladwala zomwe zimamulepheretsa kugwira ntchito.
“A Chigwenembe adakwatira mkaziyo chaka chatha koma wakhala akudwaladwala zomwe zimachititsa kuti adzilephera kugwira ntchito za pakhomo, izi sizimasangalatsa malemuwo omwe anadzimangilira pogwilitsa ntchito nsalu”,anatero Kandiado.
Zotsatira za kuchipatala zawonetsanso kuti a Chigwenembe adamwalira kaamba kobanika.
Anthu anayi akuti ndi omwe afa podzimangilira pomwe asanu afa pomira m'madzi chaka chino chokha m'bomalo.