Likulu la Mpingo wa Katolika ku Vatikani lalengeza kuti msonkhano oyamba wa makadinala okonzekera
kusankha Papa watsopano uchitika pa 4 March 2013.
Malinga ndi Chikalata chomwe mkulu wa makadinala omwe asankhe papa watsopanoyo watulutsa Kadinala Angelo Sodano, pali chiyembekezo choti pa tsikuli makadinala akhoza kutchula tsiku loyambira mwambo osankha Papa watsopanoyo.
Papa Benedicto wa 16 opuma adatula pansi udindo wake pa 28 February mwa zina kaamba koti wakula ndipo alibe mphamvu zotha kugwira bwino ntchito yotsogolera Mpingowu.