Mtsogoleri wampingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco akuyembekezeka kukacheza mdziko la Central African Republic mmwezi wa November chaka chino.
Pothilirapo ndemanga zaulendowu, Archepiskopi Dewudone Nzapalainga wa mdzikolo, wati ulendowu usonyeza chikondi chosasimbika chomwe Mulungu wawonetsa ku dzikolo lomwe lakhala lili pankhondo kwanthawi yayitali.
Ambuye Nzapalainga wati pakadali pano nkhondo yomwe idali mdzikolo yayamba yayima ndi thandizo la asilikali a bungwe la United Nations pomwenso Papa akuyembekezeka kufika mdzikolo.
Iye wati pali chiwopsezo choti a United Nations akachoka mdzikolo nkhondoyo itha kuyambiranso.
Anthu oposa zikwi makumi atatu akukhala mmisasa mdzikolo kaamba ka nkhondoyo.