Mtsogoleri wampingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco, wapempha ansembe kuti azidzipereka kwa akhristu awo amene akufuna kulapa, maka munyengo ino ya Lenti.
Papa Francisco wapereka pempholi dzulo polankhula kwa nthumwi zomwe zinali nawo pamaphunziro a pachaka okhudza sacrament lakulapa ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Mtsogoleri wampingo wakatolikayu,wati kudzipereka kwa ansembe kwa akhristu omwe akufuna kulapa, kungathandize akhristuwa kukonzekera bwino kulandira chikondi chenicheni cha Mulungu chomwe chimagonjetsa zoyipa zonse za dziko lapansi.
Iye wati masacramenti, ndi njira yokhazikika yomwe Mulungu, adaika pofuna kuyandikana komanso kukhululukira anthu, ndipo wati mpofunika kuti akhristu adziyesetsa kukwaniritsa masacramentiwa kuti alandire chikondi chake.
Iye wati kulapa kukuyeneranso kukhala phunziro kwa ansembe,amene ali mboni za anthu amene amalapa,ndipo wati izi zithandizenso iwo eni pokonza moyo wawo.