Boma la Malawi lati lifufufuza ndi kumanga anthu omwe adatsogolera ana a sukulu omwe adachita ziwonetsero zokwiya ndi kuima kwa maphunziro pamene aphunzitsi mumzinda wa Blantyre amachita nawo sitiraka yokakamiza boma kuti liwakwezere malipiro.
Boma lanena izi pa msonkhano wa a atolankhani womwe nduna ya zamaphunziro Mai Unice Kazembe inachititsa dzulo pamodzi ndi nduna yoona kuti palibe kusiyana pakati pa amai ndi a bambo komanso nduna yazamasewero ndi chitukuko cha achinyamata mu mzinda wa Lilongwe.
M’mawu awo olemekezeka mai Kazembe ati ndi okhudzidwa kwambiri ndi sitiraka yomwe anawo anachita, pomwenso katundu wa anthu osiyanasiyana wabedwa.
“Boma lichitapo kanthu msanga pofuna kuonetsetsa kuti ufulu wa ana omwe anagwiritsidwa ntchito ndi anthuwo watetezedwe”, watero Kazembe.
Ndunayi yapempha a Malawi onse kuti agwirane manja polimbana ndi mchitidwewu.
Mumzinda wa Blantyre anawa aphwanya sitolo ina pamalo omwetsera mafuta a Puma pa Kudya
ndikuba katundu .