Abwenzi a Radio Maria awapempha kukhala zitsanzo zabwino pokondana ndi kulimbika
pogwira ntchito zothandiza wayilesiyi.
Wachiwiri kwa wamkulu owona za ma Pulogalamu ku wayilesiyi, Bambo Medrick Mulava ndiye wanena izi pamwambo wa msembe ya Ukaristiya womwe cholinga chake chinali kupereka ma Khadi a umembala wa abwenzi a Radio Maria omwe unachitikira ku Parish ya Don Bosco mu Archdayosizi ya Lilongwe.
M'mau awo Bambo Mulava ati abwenzi a wayilesiyi akuyenera kutengera chitsanzo cha a Mayi Maria pokonda kupemphera ndikudzichepetsa kuti ntchito zawo zotukula Radio Maria zidziyenda bwino.
“Moyo wa mapemphero ungatithandize kuti tikhaledi mboni zenizeni za uthenga wa Mulungu
kamba koti Radio Maria imalimbikitsa kwambiri kudalira Mulungu”, atero Bambo
Mulava.
Bambowo ati monga bwenzi wa Radio Maria adzidzipereka kwathunthu komanso osabwerera m’mbuyo
ndizofooketsa zomwe angakumane nazo pamene akugwira ntchito zawo zotukula wayilesiyi.
Ndipo mkulu owona ntchito zotukula Radio Maria a Emmanuel Kaliyati wapempha abwenziwa kuti ayikonde wayilesiyi poyithandiza Radio Maria Malawi pachuma kamba koti wayilesiyi siyichita malonda ena aliwonse kuti izipeza chuma.
“Monga tonse tikudziwa kuti wailesiyi sichita malonda , tikuyenera kuti tiikonde poithandiza ndi chuma chanthu”, watero Kaliati.
Anthu 98 ochokera m’maparishi osiyanasiyana mu Archdiyosizi alandira ma Khadi aumembala
Pamwambowu panafika ena mwa akuluakulu awayilesiyi monga mkulu woyendetsa ntchito za wayilesiyi a Charles Malunga komanso Pulezidenti wa Radio Maria Malawi .