Mwambo woyika m’manda thupi la Malemu Bambo Henry Chaona omwe adamwalira pa 2 March kuchipatala cha Malamulo mu mzinda wa Blantyre uchitika pa 4 March 2013.
Likulu la diocese ya Zomba ndi lomwe lalengeza izi kudzera m’chikalata chomwe latulutsa.
Bambowa adapita nawo ku chipatalacho pa 22 mwezi wathawu ndipo pa 27 February madotolo adawapeza ndi chifuwa chachikulu cha TB. Malinga ndi chikalatacho Bambo Chaona akhala akutumikira m’maparishi osiyanasiyana ndipo amwalira akutumikira ngati mkulu woyang’anira Child Jesus Minor
Seminary ku Nankhunda .
Chikalatacho chati malemu Bambo Chaona analinso wa pa mpando wa ansembe a chibadwiri mu diocese ya Zomba.
Bambo chaona anabadwa pa 21 January m’chaka cha 1969 ndipo amachokera m’mudzi mwa Buleya kwa mfumu yaikulu Chikowi, m’parishi ya Thondwe mu diocese ya Zomba.
Mwambo yoika m’manda nthupi la malemu Bambo Chaona uchitikira ku Sacred Heart Cathedral mu diocese yomweyo ya Zomba.
Mzimu wa Bambo Henry Chaona uwuse mu mtendere wosatha.