Episkopi wa dayosizi ya Chikwawa ya mpingo wa Katolika wolemekezeka Ambuye Peter Musikuwa, wapempha ansembe ndi akhristu eni ake kuti azipempherera anthu amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana pa chikhristu ndi miyoyo yawo .
Ambuye Musikuwa , apereka pempholi Lolemba pamwambo wodalitsa mafuta womwe unachitikira ku St Michaels Cathedral mudayosiziyo.
Ambuye Musikuwa apemphanso ansembe, kuti apitilize kudzipereka pa utumiki wawo womwe adagawana ndi Yesu Khristu, poyang’aniranso kuti mwa iwo, anthu okhulupirira amawonamo Mulungu.
Iwo ati akhristu ambiri akuvutika m’maiko osiyanasiyana chifukwa chachikhulupiriro chawo, komanso pali ena amene akuvutika chifukwa cha ngozi zogwa mwadzidzidzi omwe akufunika thandizo ndinso kumawakumbukira m’mapemphero pofuna kuwalimbitsa mtima.
Mwambo wodalitsa mafuta mu mpingo wa Katolika umachitika Lachinayi m’Mlungu Woyera, koma madayosizi amapatsidwa mwayi wochita mwambowu pa tsiku lomwe asankha m’mulungu-wu lisanafike tsiku Lachisanu loyera.
Pamwambowu,ansembe mudayosiziyo abwerezanso malumbiro a utumiki wawo popempha mzimu Woyera kuti uwatsogolere.