Mapemphero ati ndi njira yokhayo yomwe ingathandize aphunzitsi kugwira ntchito yawo yophunzitsa ndi kulangiza ana a sukulu pa nkhani yokhudza umoyo wa thupi ngakhalenso wa uzimu posayang’anira mavuto omwe amakomana nawo pomwe akugwira ntchitoyi.
Bambo Henry Chimkanda otumikira mpingo wa Katolika mdziko muno ndi womwe anena izi pambuyo pa m’bindikiro wa tsiku limodzi wa aphunzitsi a m’sukulu za sekondale za chikatolika mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo ati aphunzitsi akuyenera kukhala ozama pa chiphunzitso cha mpingowu kamba koti ndi amene ali ndi udindo waukulu wogwira ntchito yozamitsa chiphunzitsochi kwa ena .
Mmodzi mwa aphunzitsi omwe anali nawo pa m’bindikirowu a Paul Chikwekwe ati m’bindikirowu wawathandiza kuti azame mu chikhristu chawo maka pomwe akugwira ntchito zawo .
Ku m’bindikirowu kunafika aphunzitsi osachepera makumi asanu ochokera msukulu za sekondale za mu mzindawu.