Pamene akhristu mdziko muno akuchita chikondwelero cha kuuka kwa Yesu Khristu, amayi a mpingo wakatolika ku parish ya St Martin ku Chirimba mu Archdiocese ya Blantyre, anachita mwambo wotolera thandizo lomwe apereka kwa akhristu ovutika a mparishiyi.
Wapampando wa bungwe la amayi mparishiyi Mayi Joana Phiri ndiwo alankhula izi potolera thandizoli.
Iwo ati achita izi pofuna kukondwelera limodzi ndi anthuwa mu nyengo ino ya pasaka. Ena mwa anthu amene apeza nawo thandizoli ndi monga okalamba ndinso ena mwa amene anakhudzidwa ndi ngozi za kusefukira kwa madzi.
Polankhula ndi mtolankhani wa Radio Maria, Mayi Joana Phiri ati anachiona chanzeru kuthandiza anthu osiyanasiyana ndi chakudya maka amene anataya katundu wawo chifukwa cha kusefukira kwa madzi.
Iwo ati monga munyengo ino ya pasaka pamene tikukumbukira kuuka kwa Ambuye anthu Yesu Khristu, tikuyenera kuwafikira anthu ena omwe akusowa chakudya chifukwa cha ngozi ya kusefukira kwa madzi komanso okalamba.