Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Akuchitidwa Chipongwe Chifukwa Chosowa Chipatala

$
0
0

Anthu okhala mdera la Kachere mu mzinda wa Blantyre adandaula chifukwa cha kusowa kwa Chipatala chaching`ono chothandiza anthu m’deralo, maka amayi omwe akuti amayenda mtunda wawutali akafuna thandizo la Chipatala.

Anthuwa apereka dandauloli pa msonkhano omwe bungwe la Concerned Youth la m’deralo, linachititsa pa nkhani zokhuza umoyo wabwino ndinso ukhondo. Msonkhanowo wachitika pamene bungweli lili mkati moyendera madera omwe anthu amakhala mothithikana m’mizinda ikuluikulu  m’dziko muno.

Iwo ati deralo likufunika chipatala chaching’ono pofuna kuchepetsa mavuto omwe  akukomana nawo. Kupatula vuto lakusowa kwa Chipatala chaching’ono m’deralo, boma la Blantyre lili ndi  Chipatala Chaboma Chimodzi cha Queen Elizabeth Central chomwe chimathandiza anthu ochokera m’maboma osiyanasiyana.

Polankhula ndi mtolankhani wa Radio Maria nkulu wa Bungwe la Corcern Youth Organization a Harvey Chimaliro anati, bungwe lawo lankhala likuphunzitsa anthu mmadera omwe anthu amakhla mothithikana kwambiri ubwino osamalira madera awo, komanso kufunsa anthu za zitukuko zomwe akuzisowa mmadela awo.

Ndi udindo wa mdzika mdera lawo kusamalira malo omwe akukhala poonetsetsa kuti zinyalala sizikutaidwa penepaliponse ,anatelo a Chimaliro.

Mayi Magombo womwe ndi mmodzi mwa dzika za kwa Kachere  anati, akusowa kwambiri Chipatala chaching’ono mderalo chifukwa zipatala zina ziri kutali ndipo anthu akhala akuchitidwa zipongwe popita ku zipatala zinazo maka ukakhala usiku.

Polankhula pa nkhaniyomweyi ,mneneri wa nkosola ya mzinda wa Blantyre a Anthony Kasunda anati akufufuza pomwe pepholi liri.

Kachere ndi limodzi mwa madera kumene anthu amakhala mothithikanaka mu mzinda wa Blantyre.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>