Apolisi mdziko la Italy amanga anthu khumi ndi asanu a chisilamu omwe akuwaganizira kuti agwetsera akhristu khumi ndi awiri mmadzi pakusamvana komwe kunabuka m’boti lomwe anakwera paulendo opita ku Italy kudzera pa Nyanja ya Meditterrenean.
Akhristuwo omwe pano akuwakaikira kuti amwalira ndi a mmaiko a Nigeria ndi Ghana.Anthu makumi anai akuwaganiziranso kuti afa boti lomwe anakwera litamila paulendo opita ku Italy.
Anthu oposa chikwi chimodzi akhala akupulumutsidwa masiku apitawa pangozi zosiyanasiyana za pamadzi pomwe amayeselera kulowa mmaiko akuulaya kudzera panyanja.