Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wapempha ma episikopi a dziko la Kenya kuti adzipereke pautumiki wawo,pofuna kuti cholinga cha mpingowu pokhala chida chachiyanjano komanso chilungamo ndi mtendere chikwaniritsidwe.
Papa Francisco wapereka pempholi lachinai pamkumano omwe anali nawo ndi ma episkopiwo kulikulu la mpingowu ku Vatican, paulendo omwe ma episkopi mumpingowu amakhala nawo pakatha zaka zisanu okacheza kulikululo,wa Adilimina.
Mtsogoleri wampingo wakatolikayu wapemphanso ma episkopiwo, kuti alimbikitse ntchito yozindikiritsa akhristu awo nkhani za chiitanidwe, ndipo ati ngakhale mphatso ya utumiki mumpingo imakhala yobadwanayo, makolo komanso aphunzitsi a msukulu zosulira atsogoleri a mpingo, ali ndi udindo waukulu owonetsetsa kuti achinyamata omwe avomera chiyitanidwe mumpingo akwaniritse zolinga zawo. Iye wayamikira ntchito zomwe mpingowu ukugwira mdzikolo maka mmagawo azaumoyo,maphunziro ndi zina.