Wapampando wa bungwe la achinyamata ku mphakati wa St Teleza ku parish ya St Francis mu Archdiocese ya Lilongwe a Kodwani Cornelius Zalimba, wati achinyamata m’dziko muno akuyenera kusintha makhalidwe awo ndi kuyamba kudzipereka pa ntchito zotukula mpingo ndi dziko lino.
A Zalimba anena izi pomwe achinyamata amphakatiwo, amapeleka thandizo losiyanasiyana kwa amayi oyembekezekera amene akulandira thandizo lawo pachipatala cha boma ku Area 25 mu m’dzindawu. Iye wati achinyamatawo, apeleka thandizolo pachipatalachi, pofuna kusonyeza mtima wachikondi pakati pa amayi amene amadzipeleka pogwira ntchito zosiyanasiyana pachisamaliro cha wanthu.
Polankhula ndi Mtolankhani wa Radio Maria Malawi a Zalimba ati anachiona chanzeru kuthandiza amayiwa chifukwa ndi amene amatenga gawo lalikulu posamalira moyo wa munthu.
Iwo analimbikitsanso achinyamata kugwira ntchito.
Tilimbikitse achinyamata onse kumene ali kuti azikonda kungwira ntchito, ngakhale yochepa motani pofuna kutukula mpingo ndi dziko lathu anatelo a Zalimba.
Achinyamatawa anapereke katundu wa ndala zosachepera 70,000 Kwacha.