Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dziko la Malawi Lisainira Mgwirizano wa Za Malonda

$
0
0

Mgwirizano wa malonda omwe wachitika pakati dziko lino ndi dziko la Tanzania, akuti uthandiza kwambiri pa chitukuko cha za malonda m’dziko muno.

Nduna ya za malonda ndi mafakitale olemekezeka a Joseph Mwanamveka, anena izi lachisanu mu m’dzinda wa Lilongwe pomwe dziko lino limasainirana panganoli ndi dzikolo.

Iwo ati unduna wawo uli ndi chikhulupiliro choti mgwilizanowu uthandiza kuti mayiko awiriwa, adzitha kulumikizana mosavuta pankhani zokhudza malonda.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi a Mwanamveka ati mabungwe awiriwa akuyenera kugawana ukadaulo osiyanasiyana pankhanizokhuza malonda.

“Pali makampani ena omwe akupanga zinthu zoononga miyoyo yanthu, tikuwachenjeza kuti asiiretu mchitidwewu chifukwa akangopezeka malamulo azangwira ntchito pa iwo,” anachenjeza a Mwanamveka.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>