Dayosizi ya Mangochi ya mpingo wa Katolika yayamikira akhristu a mpingowu komanso anthu akufuna kwabwino a mu dayosizi ya Zomba ndi Dedza, kamba kopereka thandizo la chakudya ndi zovala kwa anthu omwe adakhudzidwa ndi madzi osefukira ku Ulongwe mu dayosiziyi.
Nduna ya episkopi wa dayosiziyi Monsignor Andrew Nkhata ndi yomwe yayamikira akhristuwa Lachiwiri pamwambo wogawa katunduyu kwa anthuwa ku Ulongwe m’boma la Balaka.
Pamwambowu,Monsignor Nkhata apempha anthu omwe alandira thandizoli kuti atengerepo phunziro kwa anthu akufuna kwabwino omwe apereka thandizoli kuchokera m’boma la Zomba kudzera kubungwe lowona zachitukuko mumpingowu la Cadecom mudayosizi ya Mangochi, kuti tsiku lina adzathe kudzipereka pothandiza anzawo ndi zochepa zomwe ali nazo akadzakhala mmavuto .
Thandizoli ladza, bungwe la maepiskopi mdziko muno litapempha thandizo kudzera mmadayosizi lopita kwa anthu omwe adakhudzidwa ndi madzi osefukira.
Mmawu ake mlembi wamkulu wa bungwe la Cadecom mudayosizi ya Mangochi a Peter Nthenda,wati bungweli mu dayosiziyi likuyesetsa kuzindikiritsa anthu njira zomwe angatsate kuti athe kukhala odzidalira mmabanja awo, kudzera mu njira zosiyanasiyana kuphatikizapo kasamalidwe ka zachilengedwe pofuna kupewa ngozi za madzi osefukira.
Polankhulapo Episkopi wadayosizi ya Mangochi ambuye Montfort Sitima atsindika zakufunika koti anthu omwe akulandira thandizo kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino, azidzipereka pogwira ntchito kuti adzikala odzidalira, komanso kuti azitha kugawana ndi ena zochepa zomwe ali nazo.