Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco, akuyembekezeka kukumana ndi Pulezidenti wa dziko la Cuba a Raul Castro ku likulu la mpingowu la Mulungu likudzali.
Malinga ndi uthenga womwe a likulu la mpingowu ku Vatican atulutsa, omwe wasayiniridwa ndi mkulu wofalitsa nkhani ku likululo Bambo Federico Lombardi mkumanowu ukuyembekezeka kukhala wachinsinsi.
Mwazina Pulezidenti Castro akukathokoza Papa pa mgwirizano womwe anadzetsa pakati pa dziko lake ndi la America pa kusamvana komwe kunalipo mzaka za mma 1950 ndi 1960.
Papa Francisco akuyembekezeka kukayendera mayiko a America ndi Cuba mmwezi wa September chaka chino.