Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Anayi Afa Mdziko la Burundi

$
0
0

Anthu anayi aphedwanso pa ziwawa zomwe zikuchitika mdziko la Burundi pamene anthu akumbali yotsutsa boma akukana kuti mtsogoleri wa dzikolo ayimenso kachitatu pachisankho chomwe chichitike mdzikolo mwezi wa mawa.

Ziwawazo zikupitilira pulezidenti Pierre Nkuruzinza atatsimikizira anthu mdzikolo kuti pamene chipani chake cholamula chamusankha kuti ayimenso paudindowu pa chisankhocho, iye sadzayimanso kachinayi pa chisankho chomwe chingadzachitikenso mtsogolo.

Bungwe la mgwirizano wa mayiko a mu Africa la African Union (AU) lapempha pulezidenti Nkuruzinza kuti asayimenso pachisankhocho mwezi wa mawa.

Wampampando wabungweli mai Nkosazana Dlamini-Zuma wati chisankhocho sichichitika pamene ziwawazo zikupitilira.

Padakali pano nduna zinayi za  mmayiko anayi omwe achita malire ndi dzikolo zili mdzikolo pofuna kupeza njira zothetsera ziwawazo.

Anthu khumi,asanu ndi awiri  afa pa ziwawa zomwe zikuchitika mdzikolo pafupifupi tsiku lililonse.

Mdziko la Burundi mwakhala muli nkhondo yapachiweniweni yomwe idatha mchaka cha 2005 ndipo malinga ndi malipoti, ziwawazi  ndi zoyamba kuchokera pomwe nkhondoyo idatha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>