Mpingo wakatolika mdziko muno wati malemu Bambo Henry Kaleso omwe akhala akugwira ntchito zoyendetsa dayosizi ya Zomba, anali munthu odzipereka kwambiri pantchito zotumikira mpingo komanso anthu.
Wapampando wa bungwe la maepiskopi mdziko muno olemekezeka Ambuye Thomas Luke Msusa, omwenso ndi arkepiskopi wa arkdayosizi ya Blantyre,ndi omwe anena izi lachisanu pamwambo wa nsembe ya misa yotsazikana ndi thupi la malemuwo ku Zomba Cathedral.
Ambuye Msusa apempha atumiki onse a Mulungu kuti atengere chitsanzo cha moyo wa malemu Bambo Henry Kaleso omwe anali odzichepetsa komanso olimbikira pa utumiki wawo.
Pothilirapo ndemanga mmodzi mwa ansembe achibadwiri mudayosiziyo bambo Enerst Makande ati panthawi imene dayosizi ya Zomba ikupitiliza kukhala opanda episkopi, bambo Kaleso akhala akudzipereka kwambiri pantchito zosiyanasiyana kuti dayosiziyo ipitilize kutumikira anthu.
Iwo ati mwa malemu Bambo Kaleso atumiki osiyanasiyana aphunzira zinthu zambiri kuphatikizapo utsogoleri.
Malemu Bambo Henry Kaleso amwalira lachitatu pachipatala cha Adventist mumzinda wa Blantyre atadwala matenda a shuga kwa nthawi yochepa.
Iwo anabadwa pa 31 March mchaka cha 1959 ndipo amkachokera mmudzi mwa Kachikuni kwamfumu yayikulu Nsamala m’boma la Machinga.
Iwo anadzozedwa unsembe pa 22 August 1987 ndi Ambuye Allan Chamgwera opuma,omwe panthawiyo anali episkopi wa dayosizi ya Zomba.
Mawu awo owawunikira pa utumiki wawo mu unsembe anali oti “Motero Yesu ngakhale adali mwana wa Mulungu adaphunzira kumvera pakumva zowawa”,omwe ndi mawu ochokera pa Aheberi 5 ndime ya 8.