Akhristu omwe ali paulendo okamphera ku malo oyera ku Yerusalemu chaka chino awapempha kuti adzapite ku malowa ndi cholinga chimodzi chokapemphera kuti ayambe moyo watsopano.
Mtsogoleri waulendowu Bambo Joseph Kimu omwenso ndi mkulu owona za mapulogalamu ku Radio Maria Malawi ndi omwe apereka pempholi loweruka pa msonkhano oyamba omwe anthu omwe amaliza kulipira zofunikira zonse zaulendowu anali nawo ku St John Guest House m’boma la Mangochi.
Iwo ati maulendo okapemphera mmalo oyera ndi ofunikira kwambiri pa moyo wawuzimu kamba koti amapereka mwayi kwa akhristu opemphera momvetsetsa chikhulupiliro chawo podziwonera okha malo omwe nkhani zikuluzikulu zomwe zimapezeka mmalembo oyera zidachikira.
Mayi Agness Katsonga Phiri ndi wapampando oyang’anira anthu onse omwe akhale paulendowu ndipo anagwirizana ndi Bambo Kimu popempha anthuwa kuti adzapite kumalowa ndi cholinga chimodzi chokapemphera
Akhrisituwa adzanyamuka mdziko muno lachitatu pa 17 June, 2015 ndipo adzakhala akuyendera malo osiyanasiyana oyera mumzindawo kwa masiku asanu.

↧