Dziko la South Africa labweza anthu oposa mazana anayi 400 a mdziko la Mozambique omwe amakhala mdzikolo alibe zitupa zowayenereza.
Dzikolo lachita izi pambuyo pa ziwembu zomwe mzika za dzikolo zakhala zikuchitira anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo, zomwenso zaphetsa anthu oposa asanu ndi awiri.
Dziko la South Africa latumiza mzika za ku Mozambique-zo kwawo, apolisi mdzikolo atakhwimitsa ntchito pochita chipikisheni ndi cholinga chofuna kumanga anthu omwe akukhala mdzikolo mosavomerezeka.
Anthu ambiri amene akusowa ntchito mdziko la South Africa amadzudzula mzika za mmayiko ena zomwe zikukhala mdzikolo kuti ndi zomwe zikuchititsa kuti iwo azisowa ntchito.
Padakali pano dziko la Mozambique lati ndi lodabwa ndi kubwezedwa kwa mzika zake pamene mayiko awiriwa akuyembekezeka kukambirana nkhani yokhudza ziwawa zomwe anthu amachita mdziko la South Africa zomwenso zidaphetsa mzika yake imodzi.