Dziko la Burundi lapempha mzika za dzikolo kuti zipereke ndalama zothandizira pa chisankho chomwe chikuyembekezeka kuchitika mdzikolo mwezi wa mawa.
Izi zadza pomwe bungwe la mgwirizano wa maiko aku ulaya la European Union (EU) layimika thandizo la ndalama zoposa 2 million dollars zomwe limayenera kupereka pothandizira kuyendetsa chisankhocho.
Anthu mdzikolo akhala akuchita ziwonetsero posagwirizana ndi mfundo yoti mtsogoleri wadzikolo Pierre Nkuruzinza loti apikisane nawo kachitatu paudindo wa pulezidenti.
Pulezidenti Nkuruzinza wati iye akuyenera kupikisana nawo pa chisankhocho kamba koti mzaka zake zoyamba kukhala pa udindowu anachita kusankhidwa ndi aphungu akunyumba yamalamulo ndipo chisankho chomwe chidzachitike mdzikolo mwezi wa mawa kwa iye chidzakhala chachiwiri kuvoteredwa ndi anthu onse.