↧
Dayosizi ya Mangochi Yakhazikitsa Ntchito Yothandiza Anthu omwe Anakhudzidwa ndi Ngozi ya Kusefukila
↧
Dayosizi ya Mangochi yakhadzikitsa ntchito yopereka thandizo kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngozi za kusefukira kwa madzi
Mwambo wokhazikitsa ntchitoyi wachitikira pa msasa umene anthuwa akukhala m’mudzi mwa a GroupVillageHeadman Changamire m’dera la mfumu ya yaikulu Chimwala m’boma la Mangochi.
Polankhula pokhazikitsa ntchitoyi a VicarGeneral a Dayosiziyi bambo AndrewNkhata omwenso anayimira a episkopiaDayosiziyi ati mpingo wakatolika wakhazikitsa ntchitoyi pofuna kuchepetsa ena mwa mavuto omwe anthuwa akupitilira kukumana nawo pa msasawu ndi mmadera ena.
Bungwe la zachitukuko mu mpingowu la Cadecom ndi limene likutsogolera ntchitoyi.