Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PAPA FRANSIS SAGWIRIZANA NDI MAUKWATI AMUNA KAPENA AKAZI OKHAOKHA

$
0
0

 

Malipoti a catholic World News ati ngakhale kuti mtsogoleri wa mpingo wakatolika Papa Fransis ali omasuka  mu zambiri, sakugwizana kwambiri ndi  maukwati a pakati pa amuna kapena akazi okhaokha.

 

Papa Fransis akuti wakhala akudziwika bwino kaamba kodzichepetsa komanso kuthandiza osauka koma wakhala akudzudzula mchitidwe okwatilana amuna kapena akazi okhaokha.

 

 Iye akuti wakhala akupita kukagwira ntchito za Mpingowu pokwera bus.

 

 Pomwe papayu analengeza kuti wasankha dzina loti Fransis a katolika ambiri anasangalala kaamba koti  ambiri amakonda kwambiri moyo wa Fransis woyera wa ku Assisi  yemwe anali munthu odzichepetsanso kwambiri.

 

 

Malipoti ati m'chaka cha 2005 atamwalira papa Yohane Paulo wachiwiri Papa watsopanoyi ndi yemwe anapikisana kwambiri ndi Papa Benedicto wa 16 opuma ndipo ndi amene analetsa kuti kuvotako kusapitilire ponena kuti Benedicto wa 16 adapambana panthawiyo.

 

 Mneneli wa mpingowu ku Vatican Bambo Federico Lombardi  wati dzina la Papayu ndi Fransis osati Fransis 1,iye akuti akhoza kudzatchulidwa Fransis oyamba(1) ngati patadzapezeka papa wina ( Fransis 2) wotchedwa dzina lomweli.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>