Kadinala George Mario Bergolio wa m’dziko la Argentina ndiye mtsogoleri watsopano wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse lapansi.
Kadinalayu wasankhidwa pa 13 March 2013 patangotha tsiku limodzi kuchokera pomwe makadinala 115 anayamba m’bindikiro ofuna kusankha Papa watsopano pa 12 March 2013.
Mtsogoleri watsopanoyu adzidziwika ndi dzina lakuti Papa Fransis .
Mabelu analira komanso anthu mazanamazana omwe anasonkhana ku tchalitchi cha St Peters Square analulutira ndi chimwemwe ataona utsi woyera kuchokera ku tchalitchi cha Sistine komwe makadinalawa amachitira m’bindikiro wawo osankhira papa watsopanoyo.
Papa Fransis yemwe ali ndi zaka 76 walowa m’malo mwa Papa Benedikito wa chi 16 yemwe adapuma paudindowu mwezi watha mwa zina kamba koti wakula.
Pakadali pano atsogoleri a mayiko osiyanasiyana akupereka mafuno abwino kwa Papa Fransis.