Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mavolotiya aku Radio Maria Awalangiza Kusogoza Mulungu Pamene Akutumikira ku Wailesiyi.

$
0
0

Ma Volontiya wotumikila ku Mangochi Studiyo ya Radio Maria awalangiza kuti adzitsongoza  Mulungu pamene akugwila tchito yotumikila kufalitsa uthenga wa Mulungu kudzela pa wailesiyi.

Bambo Elizeo  Mtendere   ananena izi  Loweruka pa bindikilo womwe  unachitikila ku Seminale yaying’ono ya St Paul  ku Mangochi.

Bambo Mtendere analimbikitsa otumikila ku wailesiyi kuti adzidalila Mulungu pa zonse chifukwa chakuti,mwaiwo wonkha sangakwanitse.

“ Nyumba yomwe Ambuye samanga oyimanga ayimanga chabe”. Anatelo Bambo Mtendere.

Bambo Mtendere anayamikila utumikilawa pa ntchito yomwe amagwila yonthandiza  kufalitsa unthenga wabwino Kudzera pa Wilesiyi.

Iwo anapitiliza kunena kuti kudzela pa  Radio Maria miyoyo ya anthu ambiri ikusinthika ndipo nkoyenela kuti anthu amene akutumikila ku wailesiyi azionesa mankhalidwe abwino komanso azikonda kupemphera.

Mbindikirowu   umakozedwa  pakantha miyezi itatu iliyonse ndi cholinga chofuna   kuzamitsa moyo wa uzimu wa anthu otumikira ku wailesiyi.

Ndipo Mutu wa Mbindikilowu unali woti “Kodi Anthu Amati Ndine Yani”,Kuchokera     Mbuku Loyera pa Mateyu 16:13-19.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>