Wapampando wakomiti yowona zachilengedwe ku nyumba ya malamulo wolemekezeka a Werani Chilenga anafokozela atolankhani kuti Vuto lakusintha kwa nyengo m’dziko muno lingachepe ngati boma litayesa njila zina monga kutsitsa mtengo wa simenti, zomwe zingathandize anthu omwe amadalila mitengo akafuna kumanga nyumba.
Iwo ananea izi lachitatu pamsonkhano wa atolankhani omwe amalemba nkhani zokhudza chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo omwe unachitikila mumzinda wa Lilongwe.
"Boma likasitsa mitengo ya simenti zinthandiza kuti anthu omwe amadalila nkhuni potentha njerwa adzigwilitsa ntchito simenti powombela njerwa”. Anatelo a Chilenga.
Msonkhanowu unachitika pomwenso dziko lino likuyembekezeka kukhala ndi tsiku lokumbukira zachilengedwe omwe ukachitikire m’boma la Balaka. lachisanu.