President wa dziko lino Professor Peter Mutharika wati boma lake ndi lodzipereka pantchito yotukura maphunziro aatsikana.
President Mutharika adayankhula zimenezi pamsonkhano omwe unakonzedwa ndi bungwe la UN women omwe cholinga chake chinali kuunguza chidwi cha maiko amu Africa pankhani yothetsa maukwati a atsikana achichepere mkatikati mwa msonkhano wa bungwe la atsogoleri a m`maiko a Africa wa Africa Union.
M`mawu ake mtsogoleri wadzikolinoyu anati boma la Malawi ladzipereka kotheratu poonotsetsa kuti atsikana akukwatiwa atafika zaka 18 ndipo kuti dziko la Malawi tsopano lili ndi lamulo loti ana atsikana adzilowa m`banja atakwanitsa zaka 18 lomwe wati lakhala zaka 20 anthu asanalikambiranabe.
Ndipo anawonjezela ponena kuti boma la Malawi limanganso ma hostel aatsikana ndicholinga chochepetsa mtunda omwe anawa amayenda akamapita kusukulu.
Mmawu ake mkulu wa bungwe la UN Women Phunzile Mlambo-Ngcuka anayamikira Purezideti Muntharika kamba kachidwi chake pomenyera ufulu wa atsikana pomwe malipoti akusonyeza kuti atsikana okwana 14 million m`chigawo cha Sub Saharan Africa amachitiridwa nkhaza zosiyanasiyana .