Mwambo wa Nsembe ya Ukaristia opemphelera ulendo okayendera malo oyera mdziko la Israel wachitika lachitatu ku Parish ya St Patricks mu Arkdayosizi ya Lilongwe.
Akhristu oposa makumi anayi ndiwomwe akupita kuulendowu ndipo ena mwaiwo ndi Ansembe anayi ndi Sisiteri mmodzi.
Akhristuwa akuyembekezeka kukayendera ndi kupemphera mmalo osiyanasiyana oyera kuphatikizapo pamanda pomwe Yesu Khristu adayikidwa ndi kuuka kwa akufa.
Akhristuwa akuyembekezeka kufika mdziko muno lachiwiri pa 23 June.
Chaka ndi chaka akhristu amapita ku Malo oyera ku Yeruselemu motsogozedwa ndi Bambo Joseph Kimu womwenso ndi mkulu woyanganila Radio Maria Malawi mdziko muno.