Mtsogoleri wampingo wa Katolika padziko lonse Papa Francisco wavomereza nthumwi za mmabungwe pafupifupi makumi anai a maepiskopi zomwe zikuyembekezeka kudzakhala nawo pamsonkhano wachiwiri wa maepiskopi pankhani zokhudza banja omwe uchitike mmwezi wa October chaka chino.
Papa Francisco wavomereza nthumwizi pambuyo povomezereza zina zochokera mmabungwe 75 a maepiskopi a mmaiko osiyanasiyana omwe akuyembekezekanso kutenganawo mbali pamsonkhanowu.
Ndipo Maepisikopi a mdziko la Poland ati sazagwirizana ndi kusintha kulikonse pa chiphunzitso cha mpingo pankhani yokhudza banja pamsonkhano wa maepisikopiwa.
Ofesi yofalitsa nkhani zampingowu mdzikolo yanena izi posachedwapa pambuyo pa msonkhano omwe maepikopiwa adali nawo mdzikolo pofuna kugwirizana chimodzi ngati njira imodzi yokonzekera msonkhanowu.
Maepisikopiwa ati iwo amakhutira ndi chiphunzitso chomwe mpingowu amakhulupilira pakadali pano pankhani zokhudza banja chomwenso atsogoleri akale a mpingowu monga Papa Paulo wachinayi ndi Papa Paulo wachiwiri amkalimbikitsa.