Mayi wa zaka 62 wamwalira ndipo ena awiri awagoneka pachipatala cha Dowa atavulala kwambiri nthaka itawagumukira m’boma la Dowa.
Mneneri wa apolisi m’bomalo Sergent Richard Kaponda watsimikiza za nkhaniyi. Sergent Kaponda wati ngoziyi, yachitika pomwe anthuwa amafukula dothi lomwe amafuna kukakongoletsera nyumba zawo pa mpikisano wa mupulojekiti ina yomwe opambana akuyembekezeka kudzalandira mphotho.
Kaponda wati amayiwa ali mkati mofukula dothilo nthaka inagumuka ndi kuwaphinja ndipo mayiyo wamwalira pa malo a ngozi omwewo.
Zotsatira zakuchipatala zasonyeza kuti mayiyo Namatochi Isaac wammudzi mwa Mwaza kwa mfumu yayikulu Chiwere m’bomalo wamwalira kamba kovulala kwambiri mmutu.