Dziko la Zimbabwe lati libweza malo omwe lidalanda azungu zaka khumi ndi zisanu zapitazo pofuna kubwezeretsa phindu lomwe dzikolo limapeza paulimi omwe azungu amachita mmalowo.
Malipoti a News24 ati nduna yowona za malo mdzikolo a Douglas Mombeshora yatsimikiza kuti boma la pulezidenti Robert Mugabe lidalanda malowo ndipo lalamula kale atsogoleri onse amzigawo kuti apereke mayina a azungu omwe atsogoleriwa akufuna kuti abwezeredwe malo omwe amkagwiritsa ntchito,maka okhawo omwe akupereka chiyembekezo kuti adzathandiza potukula chuma cha dzikolo.
Malipoti akusonyeza kuti chuma cha dzikolo chidapita pansi kwambiri,mwa zina azungu atalandidwa malowo ndikuwapereka kwa mzika za dzikolo zomwe zimalephera kuwagwiritsa bwino ntchito kamba kosowa zipangizo zomwe zingawathandize kulima minda ikuluikulu.