Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Vuto la Madzi Lakula Mdera la Mchesi

$
0
0

Anthu okhala ku Mchesi m’boma la Lilongwe apempha boma kuti liyambe msanga kupereka madzi awukhondo pogwiritsa ntchito mipopi yomwe idamangidwa kale mderalo.

Malinga ndi m’modzi mwa anthu okhudzidwa mdelalo a Petias Kalichero anthu mderalo maka amayi akuvutika kwambiri kuti apeze madzi abwino, zomwenso zikukhudza kwambiri miyoyo yawo ya m’banja.

A Kalichero ati mderalo munamangidwa kale mipopi ya madzi, koma sidayambe kugwira ntchito, ndipo apempha boma kudzera ku bungwe lopereka madzi mumzinda wa Lilongwe la Lilongwe water board kuti lichitepo kanthu msanga mvula yambiri isanayambe kugwa pofuna kuti anthu mderalo adzimwa madzi awukhondo.

Iwo ati, “kuno ku Mchesi vuto la madzi ndi lalikulu kwambiri, tikuthokoza boma kuti linatimangira malo a madzi koma chomwe tikupempha ndi chakuti atithandize mwachangu kuti madzi ayambe kutuluka.”

Pamenepa a Kalichero anati ndi zomvetsa chisoni kuti amayi ambiri amadzuka usiku kukatunga madzi zomwe sizipereka ulemu ku mabanja ambiri mderali.

“Amayi akumadzuka 2 koloko ya usiku kupita kukasaka madzi zomwe chiwopsezo chake ndi chakuti mabanja amasokonekera kamba koti abambo si ambiri amene amakhulupilira kuti akazi awo apita ku madzi,”anatero a Kalichero

Pomwe Radio Maria Malawi imafuna kumva zambiri pa zomwe zikulepheretsa kuti mipope yomwe yadzalidwa mderalo iyambe kugwira ntchito,akuluakulu a ku Lilongwe water board samayankha lamya zawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>