Apolisi m’boma la Balaka apempha atsogoleri a mmagulu osiyanasiyana kuti atengepo gawo lalikulu pantchito yokhwimitsa chitetezo m’bomalo.
Mkulu owona ntchito za apolisi akumidzi m’bomalo Sub-Ispector Roster Milanzindi yemwe wapempha maguluwa lachisanu pamsonkhano omwe anakonzera magulu osiyanasiyana akumidziomwe unachitikira kulikulu la mfumu yayikulu Chamthunya m’bomalo.
Milanzi wati pamene dziko lino likukumana ndi vuto la kuchepa kwa chitetezomagulu osiyanasiyana akuyenera kutengapo gawo lalikulu pofuna kubwezeretsa chitetezo pakati pa anthu pomwe vuto la kuchepa kwa chitetezo lakula kwambiri mdziko muno.
Iye wati pofuna kukwaniritsa ntchitoyianthu akuyenera kudziwa bwino za anthu omwe amakhala nawo pafupi, ndikukanena kupolisi akakayikira chilichonse mwa iwo.
Pothilirapo ndemanga mfumu yayikulu Chamthunya yalonjeza kuti ichita chotheka pokhwimitsa chitetezo mdera lake ndipo yalimbikitsanso amayi kuti asamabise anthu omwe aphwanya ufulu wawo komanso wa ana.