Anthu khumi ndi asanu aphedwa ndinso ena khumi avulala atawomberedwa ndi anthu ena omwe anakwera ngamila mdziko la Sudan.
Mmodzi mwa anthu omwe avulala pachiwembucho wawuza atolankhani kuchipatala komwe amugoneka,kuti anthu omwe achita chiwembucho amachokera kokawona abale awo mdera lomwelo, ndipo achita izi pomwe amabwerera kwawo lachiwiri sabata ino.
Anthu a mdera lakuzambwe kwa dzikolo komwe chiwembucho chachitikira, ati amakhala mosatsata malamulo pochita zinthu zawo, kuyambira mchaka cha 2003 pamene mitundu ina ya anthu idayamba kuwukira boma lomwe limatsata kwambiri malamulo a mmayiko a chiluya, lomwe akuti limawasala kwambiri.
Anthu 300 sauzande ndi omwe aphedwa pakusamvanako,ndipo ena oposa 2 miliyoni anathawa mnyumba zawo.
Mitundu yambiri mdzikolo akuti imakanganira zinthu zofunika kwambiri pamoyo watsiku ndi tsiku kuphatikizapo madzi omwe mmadera ambiri amasowa chifukwa cha chipululu.