Banki yaikulu pa dziko lonse ya World Bank, yalonjeza kuti ipereka ngongole ya ndalama zokwana 2.1 biliyoni za America zothandiza kukonzera madera ena omwe gulu la zauchifwamba la Boko Haram lidawonga.
Malipoti a wailesi ya BBC ati mtsogoleri wadzikolo Muhhamudu Buhari, wapempha bankiyi kuti itumize nthumwi zake mdzikolo kuti zikawonerere momwe ndalamazo zingagwilire ntchito.
Iye wati ndalamazo, mwazina, zigwiritsidwa ntchito yomangira nyumba zomwe zigawengazo zidawononga, komanso kuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi zamtopola zomwe gululo lakhala likuwononga.
Pulezidenti wa dziko la America Barack Obama, walonjezanso kuti athandiza dziko lake ndi ndalama zokwana 5 miliyoni dolazi za America zolimbanira ndi gululo , potsatira chidwi chomwe pulezidenti Buhari wawonetsa pofuna kuthana ndi mchitidwe wauchifwamba mdzikolo.
Padakali pano pulezidenti Buhari walonjeza kuti achita chotheka kukambirana ndi akuluakulu a gulu la zigawengalo, pofuna kuti amasule asungwana oposa mazana awiri omwe akuwasunga mokakamiza kuyambira chaka chatha.