Bungwe la Malawi Red Cross layambitsa ntchito yolimbikitsa uchembere wabwino m’maboma a Kasungu ndi Ntchisi.
Ntchitoyi yomwe ndi ya ndalama zokwana 600 million kwacha ikuyembekezeka kuthandiza kuchepetsa imfa za amayi oyembekezera komanso ana m’mabomawo.
Ntchitoyi igwilidwa ndi thandizo lochokera ku boma la dziko la Belgia, ndipo ikuyembekezera kutha mwezi wa December.
Mkulu wa pa chipatala cha Kasungu Dr.Jeromy Nkambule athokoza bungweli kaamba kothandiza pa ntchito yolimbikitsa ntchito za uchembere wabwino m’mabomawo.