Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse lapansi Papa Francis wayamikira nyumba zofalitsa nkhani pa dziko lonse kaamba kotsatira ndi kulengeza bwino zonse zomwe zimachitika ku likulu la Mpingowu kuchokera pomwe Papa opuma Benedikito wachi 16 atalengeza zopuma paudindowu mwezi watha.
Papa Francis amankhula izi ndi atolankhula ku likulu la mpingowu ku Vatican m'dzikolo.
Iye wati nyumba zofalitsa nkhani zili ndi udindo ofotokozera anthu zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo za mu Mpingo.
Papa Francis walowa m’malo mwa Papa Benedikito wa chi 16 yemwe adapuma pa udindowu mwezi watha mwa zina kamba koti wakula.