Arkiepiskopi wa Arkidayosizi ya Lilongwe ya Mpingo wa Katolika Ambuye Remi Ste Marie apempha akhristu a Mpingowu mu arkidayosiziyo kuti alimbitse chikhulupiliro chawo pomwenso akhristu a Mpingowu pa dziko lonse ali m’chaka cha chikhulupiliro.
Ambuye Remi Ste Marie amalankhula izi pa 17 March 2013 pamwambo okondwelera komanso kukumbukira nkhoswe ya parishi ya St. Patrick’s mu arkidayosiziyo.
M’mawu awo Ambuye Ste Marie apempha akhristuwo kuti nthawi zonse adziyika chikhulupiliro chawo mwa Mulungu pofuna kupeza mayankho owona pa zosowa zawo.
“Chikhulipiriro chili ngati khomo lolowera ku chipulumutso ndipo munthu yemwe ali ndi chikhulupiriro amalandira madalitso ochuluka. N’koyenera kuti akhristu tiwonetse chikhulupiliro chozama pochita ntchito zabwino, tidziwerenga Baibulo komanso Katekisimu wa Katolika kuti chikhulupiliro chathu chikule”, anatero Ambuye Ste Marie.
Chaka cha chikhulupiliro mu Mpingo wa Katolika chinayamba pa 11 October 2012 ndipo chidzatha pa 24 November 2013.