Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lati layimitsa ganizo lake lofuna kugwiritsa ntchito makina atsopano pa kalembera wa voti pokonzekera chisankho cha m’magawo atatu chomwe chichitike chaka cha mawa.
Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati ganizoli ladza potsatira malangizo omwe akatswiri osiyanasiyana pa zisankho apereka ku bungweli pa nkhani yofuna kugwiritsa ntchito makina atsopanowo.
Chikalatachi chati makinawa atha kudzagwiritsidwa ntchito pa chisankho china chomwe chidzachitike m’chaka cha 2019. Radio Maria Malawi Online