Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wakhazikitsa tsiku la pa 1 September chaka chino kuti likhale lopemphelera chisamaliro cha chilengedwe.
Papa Francisco wakhazikitsa tsikuli pa msonkhano womwe anali nawo ndi akuluakulu a mabungwe a Utumiki wa Chilungamo ndi Mtendere ndi Wolimbikitsa Umodzi pakati pa akhristu mu mzinda wa Rome.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya mpingo wakatolika ku likulu la mpingowu ku Vatican, Papa wakhazikitsa tsikuli pofuna kulimbana mokwanira ndi mavuto omwe anthu akukumana nawo kamba kakuwonongeka kwa chilengedwe komwe kukudzetsa mavuto akusintha kwa nyengo.
Papa wati akhristu patsikuli akuyeneranso kutenga gawo lalikulu pothokoza Mulungu pa chisamaliro komanso chitetezo chapadera chomwe amalandira mwa Mulungu kaamba koti nawonso ndi mbali imodzi ya chilengedwe.