Mfumu yayikulu ya Angoni mdziko la South Africa Goodwill Zwelithini ikuyembekezeka kufika mdziko la Zimbabwe masiku akudzawa.
Magulu osiyanasiyana omenyelera ufulu wa anthu mdziko la Zimbabwe ati mfumu Zwelithini ndi yolandiridwa mdzikolo ngakhale yakhala ikudzudzulidwa kuti ndi yomwe idachititsa kuti mzika za dziko la South Africa ziyambe kuchitira nkhanza anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo pazifukwa zosiyanasiyana kumayambiliro a chaka chino.
Padakali pano bungwe lowona za maufulu a wanthu mdzikolo la South African Human Rights Commission likupitiliza kufufuza mfumuyi kamba ka zomwe idalankhula m’mwezi wa March chaka chino pa msonkhano omwe idachititsa mumzinda wa KwaZulu-Natal pomwe idanena kuti anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo abwelere mmayiko awo.
Anthu asanu ndi awiri adaphedwa pa ziwawa zomwe zidabuka potsatira zomwe mfumuyo idanena.
Mfumuyi ifika mdzikolo kumapeto a mwezi uno itayitanidwa ku ukwati wa mkulu wina wazamalonda wa mdziko la Zimbabwe yemwe amagwilira ntchito zake mdziko la South Africa-lo.