Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mabungwe Atenge Nawo Mbali pa Nkhani ya Magetsi

$
0
0

Kupereka mwayi ku mabungwe osiyanasiyana omwe  siaboma kutenga nawo gawo pa ntchito zokhudza magetsi mdziko muno ati kungathandize kuti  mitengo yamagetsiwa ikhale yotsikirapo.

Wofalitsa nkhani ku unduna wa zamigodi mphamvu zamagetsi zachilengedwe ndi nyama zakuthengo a Josephy Kalowekamondi womwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pomwe imafuna kumva zambiri pa nkhani yofuna kugawa pawiri bungwe logulitsa magetsi mdziko muno la   ESCOM kuti idzitha kukwaniritsa zofuna za anthu.

A Kalowekamoati anthu akuyenera kumvetsetsa kuti silikufuna kugulitsa bungwe la ESCOM koma kuti akufuna kuligawa kukhala nthambi ziwiri zomwe ndi yopanga magetsi  komanso yogulitsa magetsi pofuna kukweza kagwiridwe ka ntchito  ka bungweli.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875