Wailesi za Maria zomwe zidakhazikitsidwa kale pa dziko la pansi zakonza dongosolo lofuna kuthandiza kukhazikitsa wayilesi zina m’mayiko momwe akufuna kukhalanso ndi wayilesi za amayi Maria pa dziko la pansi.
Pakadali pano wayilesi za Maria zilipo pafupifupi makumi asanu ndi awiri (70) pa dziko lonse lapansi.
Wayilesizi zakonza ndondomeko yapadera pofuna kupezera thandizo la ndalama zugulira zida zomangira wailesi zina za Maria m’mayiko khumi ndi limodzi(11).
Mkulu owona za mapologalamu pa wayilesi ya Radio Maria Malawi Bambo Joseph Kimu ati dongosolo lofuna kupeza ndalamazi lichitika kwa masiku atatu kuyambira pa 10 mpaka 12 May chaka chino.
Pamasikuwa wailesi zomwe zidakhazikitsidwa kale zidzaulutsa mapulogalamu a padera opempha thandizo.
Bambo Kimu ati ganizoli lidapangidwa pa msonkhano wa akuluakulu omwe amayendetsa wailesizi
padziko lonse omwe udachitikira mu mzinda wa Rome.
Iwo ati Radio Maria Malawi ikuyembekezeka kupeza ndalama zosachepera 2 million kwacha.
“Tili m’dziko losauka ndipo omvera anthu sapereka kwambiri poyerekeza ndi ma wayilesi ena komabe tiyenera kuwathandiza a mzathu kamba koti ifeyo anthu ena adatithandizanso kuti wayilesi ya Radio Maria Malawi ikhazikitsidwe m'dziko muno”,atero Bambo Kimu.
Mutu omwe wasankhidwa pa masiku atatuwo ndi oti Tithandize Mai Athu,kuti Nawoso Atithandize. Radio Maria Malawi Online