Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Pulezidenti Kiir Wakana Kusayinira Mgwirizano Wodzetsa Mtendere

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la South Sudan Salva Kiir wakana kusayinira mgwirizano odzetsa mtendere pakati pa iye ndi magulu owukira boma mdzikolo.

Pulezidenti Kiir wakana kusayinira panganoli posachedwapa mumzinda wa Addis Ababa mdziko la Ethiopia komwe anakumana ndi mtsogoleri wakumbali yowukira Rik Marshal.

Boma la South Sudan layika mfundo zoyenera kutsatidwa pa mgwirizanowu koma pulezidenti Kiir wati adzasayinira pangonoli pakatha sabata ziwiri zikudzazi.

Amkhala pakati pa zokambirana zapakati pa akuluakulu awiriwa awopseza kuti mayiko ayamba kusala dzikolo ngati atsogoleri awiriwa samvana chimodzi pomafika lolemba likudzali.

Padakali pano dziko la America lapempha pulezidenti Kiir kuti asayinire pangonoli pomwe mtsogoleri wakumbali yowukirayo wasayinira kale.

Anthu zikwizikwi aphedwa ndipo ena oposa 2 miliyoni athawa mnyumba zawo pankhondo ya pakati pa mbali ziwirizi yomwe idayamba mchaka cha 2013.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>